Malawi Native Anthem Text


Mlungu dalitsani Malawi,
Mumsunge m'mtendere
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope
Mdalitse Mtsogo leri na fe,
Ndi Mai Malawi

Malawi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m'mapiri,
Ndithudi tadala
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N'mphatso zaulere
Nkhalango, madambo abwino
Ngwokoma Malawi

O! Ufulu tigwirizane,
Kukweza Malawi
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire
Pa nkhondo nkana pa mtendere,
Cholinga n'chimodzi
Mai, bambo, tidzipereke,
Pokweza Malawi
Sent by Carlos André Pereira da Silva Branco







Captcha